KUZINDIKIRA NDI KULIMBANA NDI MATENDA A NANZIKAMBE MU CHIMANGA
MAWU OYAMBA
Nanzikambe ndi matenda owononga kwambiri amene amagwira masamba a chimanga. Matendawa amafalitsidwa ndi zinthu zooneka ngati nkhungu ndipo amagwiranso mbewu zina monga mapira, mzimbe komanso mawere. Ngakhale matendawa akhala m’dziko muno kwa nthawi yayitali, alimi ambiri amalephera kuwazindikira, izi zimapangitsa kuti azifala kwambiri. Matendawa a nanzikambe ndi oopsa ndipo amapangitsa kuti alimi asakolole kalikonse m’munda.
ZIZINDIKIRO ZA MATENDA A NANZIKAMBE
- Masamba amakhala ndi mizere yachikasu imene imayamba kuoneka chimanga chikatha masiku 9 kuchokera tsiku lomwe chinamera
- Chimanga chikagwidwa ndi matendawa chikadali chaching’ono chimaoneka chokwinimbira ndipo chimatha kufa pasanadutse masabata anayi kuchokera pomwe chinagwidwa ndi matendawa
- Masamba a chimanga chikuluchikulu amakhala ndi mizere yachikasu imene imayambira pa tsinde la tsamba, ndipo mbali ya tsamba logwidwa ndi matendawa limaoneka mosiyana ndi mbali yomwe sikunafalikire matendawa
- Masamba a chimanga chogwidwa ndi matendawa amakhala osatambasuka bwino komanso oyimilira mosayenera
- Chizindikiro chodziwika bwino cha matendawa ndi nkhungu zomwe zimaoneka kunsi kwa masamba ndipo zimatha kukhala zoyera, zoyera moderako kapena za mtundu wa purple. Nthawi zambiri mu chimanga nkhunguzi zimakhala zoyera
- Chimanga chikamakula ngayaye zimapindika ndipo chimanga sichibereka
- Ngayaye zimaphimbidwa ndi masamba ambiri omwe amakula mopotana ku nsonga za chimanga
- Matendawa akalekeleredwa chimanga chimalephera kubereka
Dziwani izi: Matenda a nanzikambe ndiosiyana ndi matenda a chikanga. Chimanga chogwidwa ndi nanzikambe, mizere ya chikasu imayambira pa tsinde la tsamba kenako imafalikira mbali zonse pamene chimanga chogwidwa ndi chikanga, mizere imayambira ku nsonga kwa tsamba.
Zizindikilo zomwe zimaoneka pachimanga chomwe chagwidwa ndi matendawa
- Mtundu wa chikasu oyambira pa tsinde la tsamba
- Mbali yogwidwa ndi matenda kuoneka mosiyana ndi mbali yosagwidwa ndi matenda
- Nkhungu kunsi kwa masamba Chithunzi
- Ngayaye zogwidwa ndi matenda Chithunzi
- Masamba opotana ku nsonga ya chimanga
KUFALA KWA MATENDA A NANZIKAMBE
Njere zoyambitsa matenda a nanzikambe zimafalitsidwa ndi mphepo komanso mvula. Njerezi zimatha kukhala ku mbewu, zotsalira za zokolola komanso dothi, ndipo zimakula bwino malo a chinyontho komanso nyengo ikakhala yotentha pa mlingo wa pakati pa 21-26ºC.
KUTHANA NDI MATENDA A NANZIKAMBE
Musanabzale:
- Galauzani munda mozama bwino
- Bzalani mbewu zovomerezeka ndi Boma komanso zochokera kwa ogulitsa mbewu ovomerezeka
- Pewani kubzala chimanga pafupi ndi mzimbe popewa kufala kwa matendawa
- Pewani kubzala chimanga mosakaniza ndi mbewu zina zomwe zimagwidwa ndi matendawa
- Bzalani mbewu pa mlingo ovomerezeka kuti mphepo idzidutsa bwino m’munda
- Limani chimanga mwakasinthasintha ndi mbewu zam’gulu la nyemba
- Sakanizani mbewu m’mankhwala a Metalaxyl okwana 6g pa kilogalamu iliyonse ya chimanga
Pamene Mbewu Zamera:
- Zulani ndi kukwilira msanga mbewu zimene zagwidwa ndi matendawa
- Pewani kuyendayenda m’minda imene muli mbewu zogwidwa ndi matendawa kuti asafale
- Pewani kusiya mphukira za mapira m’munda pofuna kupewa kuchulukana kwa njere zoyambitsa matendawa.
Mukakolola:
- Tenthani kapena kwilirani zotsalira za mbewu m’munda omwe unagwidwa ndi matendawa
Mukafuna kudziwa zambiri za matendawa, kaonaneni ndi alangizi a zaulimi amene muli nawo pafupi.
